• November 29, 2022 6:31 pm

Kondwani Kachamba Ngwira , ndi Olemekezeka a Paul Nkhoma agwirana  

Nov 18, 2022
Phungu wa dela la kumpoto mboma la Kasungu Olemekezeka a Paul Nkhoma agwirana manja ndi katswiri pa nkhani yophunzitsa anthu pa ukadaulo wa malonda , Kondwani Kachamba Ngwira kuti athandize anthu powaphunzitsa luso losiyana siyana lopangira katundu.
Kachamba yemwe wakhala akuphunzutsa anthu osiyana siyana mdziko muno akhala ndi gulu lake lonse ku delali Loweruka pa 19 November, 2022, kuyambira nthawi ya 9:00 Mmawa.
Pachifukwachi a Nkhoma akumema aliyese yemwe ali ndi chidwi pa maphunzirowa kuti apite pa bwalo la zamasewera la Chatoloma ADMARC atanyamula cholembera mmanja ndi kope lomwe.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.