• November 29, 2022 5:35 pm

Phungu wadera lapakati mumzinda wa Lilongwe, Alfred Jiya, watsutsa malipoti oti akukondela pogawa zitukuko

Aug 28, 2022

Phungu wa dela la pakati mumzinda wa Lilongwe, Alfred Jiya, watsutsa malipoti omwe anthu ena akufalitsa oti zitukuko akungoponya kumadela komwe iye amakhala.

Jiya : Phungu wachitukuko

Jiya watsutsa izi Lachisanu pomwe iye amakhazikitsa ntchito yomanga mlatho pamtsinje omwe umalumikiza Chisaleka ndi Chatata.

Jiya : A Katundu

Ntchito yomanga mlathowu ikuyembekezeka kudya ndalama zoposera 43 Miliyoni kwacha.

Mlatho wa Kauma

A Jiya anati ndi khumbo lawo nthawi zonse kuti zitukuko zifalikire dela lililonse ndipo izi anati zikutheka.

Apa Jiya kuyatsa magetsi

Phunguyu anapereka zitsanzo zambiri za zitukuko zomwe zachitika m’madela ena omwe iye amayenda nthawi yokopa anthu.

A Jiya anati:

“Chimene chimachitika n’chakuti, nthawi yokopa anthu, timalandila madandu okhudza zosowa zawo kudelako. Pano tikamapereka zitukuko kumakhala kungo kwanilitsa zomwe tinatenga kale.”Jiya ndi mmodzi mwa aphungu yemwe waonetsa chidwi pankhani zotukula dela lake. Pakanthawi kochepa ali Phungu, Jiya wakwanitsa kuitanitsa zitukuko zambiri monga Mlatho wa Mchokwe, Kauma State House, Area 18, Senti, komanso Kanengo- Mgona.

Pakadali pano mfumu yaikulu Chatata yayamikila Olemekezeka a Jiya kamba kogawa zitukuko mopanda tsankho.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.